Isaiah 56:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbikira kuzichita, amene amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, ndipo amadziletsa kuchita zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, amene asunga Sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbika kuzichita, amene amasunga Sabata osaliyipitsa, ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wodala munthu amene acita ici, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ici, amene asunga sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lace osacita nalo coipa ciri conse.