Isaiah 56:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkunja amene waphatikana ndi Chauta, asanene kuti, “Mosapeneka konse Chauta adzandichotsa pakati pa anthu ake.” Nayenso wofulidwa asanene kuti, “Ine ndiye ndine wouma ngati chikuni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ake; pena mfule asanene, Taonani ine ndili mtengo wouma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti, “Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.” Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti, “Ine ndine mtengo wowuma basi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ace; pena mfule asanene, Taonani ine ndiri mtengo wouma.