Isaiah 56:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ineyo ndidzaŵapatsa dzina ndi mbiri yabwino pakati pa anthu anga, m'kati mwa fuko langa, koposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzaŵapatsa mbiri yabwino yosatha, yosaiŵalika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana aamuna ndi aakazi; ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake, kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzawapatsa dzina labwino, losatha ndi losayiwalika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana amuna ndi akazi; ndidzawapatsa dzina lacikhalire limene silidzadulidwa.