Isaiah 56:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akutinso, “Akunja amene amaphatikana ndi Chauta mpaka kumgwirira ntchito, kumkonda, ndi kumtumikira, amenenso amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, nasunga bwino chipangano changa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova, motero kuti amamutumikira Iye, amakonda dzina la Yehova, amamugwirira ntchito, komanso kusunga Sabata osaliyipitsa ndi kusunga bwino pangano langa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ace, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba cipangano canga;