Isaiah 57:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a Mulungu okhulupirira amafa, ndipo palibe amene amasamalako. Anthu okhulupirika amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amachotsedwa, kuti tsoka lisaŵagwere,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu olungama amafa, ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake; anthu odzipereka amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amatengedwa kuti tsoka lisawagwere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu acifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama acotsedwa pa coipa cirinkudza.