Isaiah 57:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudatopa nawo mtunda wouyenda, koma osanena kuti, “Ndingoleka!” Mudapezera zina mphamvu, mwakuti simudalefuke konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unatopa ndi njira yako yaitali; koma sunanene, Palibe chiyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; chifukwa chake sunalefuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumatopa ndi maulendo anu, koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’ Munapezako kumeneko zokhumba zanu nʼchifukwa chake simunalefuke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unatopa ndi njira yako yaitari; koma sunanene, Palibe ciyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; cifukwa cace sunalefuka.