Isaiah 57:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Iye amene ali wamtari wotukulidwa, amene akhala mwacikhalire, amene dzina lace ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atari ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzicepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzicepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.