Isaiah 57:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndine amene ndidalenga anthu anga ndi kuŵapatsa mpweya wa moyo, motero sindidzapitirira kukangana nawo kapena kuŵakwiyira mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindidzawatsutsa anthu mpaka muyaya kapena kuwapsera mtima nthawi zonse, popeza kuti ndinalenga anthu anga ndi kuwapatsa mpweya wamoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sindidzatsutsana ku nthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.