Isaiah 57:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse. Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa, m'ming'alu yam'mathanthwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu, ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri. Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwa ndiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?