Isaiah 57:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'nyumba mwanu mwaika mafano ku chitseko ndiponso pa mphuthu. Ine mwandisiya, mwavula zovala zanu, mwakwera pa bedi lanu lalikulu ndi zibwenzi zanu zimene mwazilipira kuti mugone nazo. Kumeneko mwakwaniritsa zilakolako zanu zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa chikumbutso chako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼnyumba mwanu mwayika mafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu. Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu. Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu, ndiye mwazilipira kuti mugone nazo. Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa cikumbutso cako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.