Isaiah 57:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudadzola mafuta ndi zonunkhira zochuluka, ndipo mudapita kukapembedza fano lija la Moleki. Mudachita kutuma nthumwi kutali, mudazituma ngakhale kumanda komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafuta ndi zonunkhira zochuluka. Munachita kutumiza akazembe anu kutali; inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kucurukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutari; ndipo wadzicepetsa wekha kufikira kunsi ku manda.