Isaiah 58:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Fuula kwambiri, usaleke, mau ako amveke ngati lipenga. Uŵauze anthu anga za kulakwa kwao, uŵauze a m'fuko la Yakobe za machimo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Fuwula kwambiri, usaleke. Mawu ako amveke ngati lipenga. Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo; uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pfuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga colakwa cao, ndi banja la Yakobo macimo ao.