Isaiah 58:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ngati upereka kwa wanjala cimene moyo Iwako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wobvutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;