Isaiah 58:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse; adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa ndipo adzalimbitsa matupi anu. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe amene madzi ake saphwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'cirala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ace saphwa konse.