Isaiah 58:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata, osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera. Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa, tsiku loyera la Chauta muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka. Muzililemekeza pakusayendayenda, poleka kugwira ntchito zanu ndiponso posakamba nkhani zachabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzisunga osaphwanya Sabata; musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika, tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo. Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekeza posayenda mʼnjira zanu, kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kucita kukondwerera kwako tsiku: langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osacita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;