Isaiah 58:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu.” Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa colowa ca kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.