Isaiah 58:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku onse iwo amaoneka ngati akufuna kuchita zimene Ine ndifuna. Amangonena kuti afuna kumvera malamulo a Mulungu wao. Amandipempha kuti ndigamule mlandu wao mwachilungamo, ndipo amakondwera kukhala pafupi ndi Mulungu wao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine; amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna, kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake. Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ocita cilungamo, osasiya cilangizo ca Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.