Isaiah 58:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akufunsa kuti, “Kodi tizisaliranji zakudya, pamene Inu Chauta simulabadako? Kodi tivutikirenji nkudzichepetsa, pamene Inu simusamalako?” Chauta akunena kuti, “Kunena zoona, tsiku limene mumasala zakudya lija, mumafunafuna zimene zingakupatseni phindu, mumazunza antchito anu onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? Ndi bwanji ife tavutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza antchito anu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala kudya pamene Inu simukulabadirapo? Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa pamene Inu simunasamalepo?’ ” Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani, ndipo mumazunza antchito anu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? ndi bwanji ife tabvutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza anchito anu onse.