Isaiah 58:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi kusala kumene ndimafuna Ine nkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Inu mumaŵerama pansi ngati udzu, mumayala ziguduli nkuthirapo phulusa kuti mugonepo. Kodi ndiye mumati kusala kumeneku, tsiku lokondwetsa Chauta?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? Tsiku lakuvutitsa munthu moyo wake? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wake monga bango, ndi kuyala chiguduli ndi phulusa pansi pake? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lovomerezeka kwa Yehova?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo? Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko, tsiku lokondweretsa Yehova?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? tsiku lakubvutitsa munthu moyo wace? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wace monga bango, ndi kuyala ciguduli ndi phulusa pansi pace? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lobvomerezeka kwa Yehova?