Isaiah 58:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna: Kumasula maunyolo ozunzizira anthu ndi kumasula zingwe za goli, kupereka ufulu kwa oponderezedwa ndi kuphwanya goli lililonse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga gori, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti mutyole magori onse?