Isaiah 58:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha, ndipo mabala anu adzachira msangamsanga; chilungamo chanu chidzakutsogolerani ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kucira kwako kudzaonekera msanga msanga; ndipo cilungamo cako cidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wocinjiriza pambuyo pako.