Isaiah 59:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Timapapasapapasa ngati anthu akhungu, tili ngati anthu opanda maso. Timaphunthwa masana ngati usiku. Ndife amoyo ndithu, komabe tili ngati anthu akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tiphunthwa usana monga m'chizirezire; tili m'malo amdima ngati akufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona, kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso. Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku; timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tipunthwa usana monga m'cizirezire; tiri m'malo amdima ngati akufa.