Isaiah 59:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; chifukwa chake mkono wakewake unadzitengera yekha chipulumutso; ndi chilungamo chake chinamchirikiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe, Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera; Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza, ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; cifukwa cace mkono wace wace unadzitengera yekha cipulumutso; ndi cilungamo cace cinamcirikiza.