Isaiah 59:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso. Adavala kulipsira ngati mkanjo, ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso; anavala kulipsira ngati chovala ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabvala cilungamo monga cida ca pacifuwa, ndi cisoti ca cipulumutso pamutu pace; nabvala zobvala zakubwezera cilango, nabvekedwa ndi cangu monga copfunda,