Isaiah 59:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake molingana ndi zimene anachita, adzaonetsa ukali kwa adani ake ndi kubwezera chilango odana naye. Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga mwa nchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ace ukali, nadzabwezera adani ace cilango; nadzabwezeranso zisumbu cilango.