Isaiah 59:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho akadzabwera ngati madzi oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho. Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco iwo adzaopa dzina la Yehova kucokera kumadzulo, ndi ulemerero wace kumene kuturukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati cigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.