Isaiah 59:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe amene amaimba mnzake mlandu molungama, palibe wopita ku bwalo lamilandu moona. Amadalira zopanda pake, amangonena mabodza. Amangolingalira zamphulupulu, nachitadi zoipa zimene akuganiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama, palibe amene akupita ku mlandu moona mtima. Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza; amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibe woturutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwacabe, nanena zonama; iwo atenga kusayeruzika ndi kubala mphulupulu,