Isaiah 59:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukonde wa kangaude sangauvale ngati nsalu, chimene anthu amapangacho sangafunde konse. Ntchito zao nzoipa ndipo amakonda kuchita zandeu ndi manja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maukonde ao sadzakhala zovala, sadzafunda ntchito zao; ntchito zao zili ntchito zoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala; ndipo chimene apangacho sangachifunde. Ntchito zawo ndi zoyipa, ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maukonde ao sadzakhala zobvala, sadzapfunda nchito zao; nchito zao ziri nchito zoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwao.