Isaiah 59:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amathamangira kukachita zoipa, sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo ao onse ali pa zoipa. Kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja, ndiponso amaononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amathamangira kukachita zoyipa; sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo awo ndi maganizo oyipa; kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosacimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi cipasuko ziri m'njira mwao.