Isaiah 59:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akuti, “Chifukwa cha zonsezo chilungamo chatikhalira kutali, ndipo kukhala aungwiro nkosatheka. Timafunafuna kuŵala, koma timangopeza mdima. Timayembekeza kuti kudzakhala mbee, koma kuli bii.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake chiweruziro chili patali ndi ife, ndi chilungamo sichitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira; ndipo chipulumutso sichitifikira. Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha; tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ciweruziro ciri patari ndi ife, ndi cilungamo sicitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.