Isaiah 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala m'Kachisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka cimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wacifumu wautari, ndi wotukulidwa, ndi zobvala zace zinadzala m'Kacisi.