Isaiah 6:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu ameneŵa uŵaphe mtima, uŵagonthetse makutu, ndipo uŵatseke m'maso, kuti angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mitima yao, kenaka nkutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu amenewa uwaphe mtima; uwagonthetse makutu, ndipo uwatseke mʼmaso. Mwina angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi mitima yawo, kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, naciritsidwe.