Isaiah 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo ine ndidati: “Tsoka langa ine! Ndatayika. Pakuti ndine munthu wa pakamwa poipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poipa. Komabe maso anga aona Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! cifukwa ndathedwa; cifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; cifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.