Isaiah 60:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuuza Yerusalemu kuti, “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu ao adzakutumikira. Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndi kukuchitira chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu awo adzakutumikira. Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakucitira iwe cifundo.