Isaiah 60:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse. Usana ndi usiku womwe sadzazitseka, kuti choncho anthu a mitundu yonse adzabwere ndi chuma chao kwa iwe, akuyenda pa mdipiti, mafumu ao ali patsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse, sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku, kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo, akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere naco kwa iwe cuma ca amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.