Isaiah 60:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini, imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni, adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga. Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini, mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanoni kuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika; ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ulemerero wa Lebano udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a kacisi wanga; ndipo ndidzacititsa malo a mapazi anga ulemerero.