Isaiah 60:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu. Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi. Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta, ndiye kuti Ziyoni, mzinda wa Woyera uja wa Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana amuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mudzi wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani; onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu. Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova; Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana amuna a iwo amene anabvuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakucepetsa iwe adzagwadira ku mapazi ako, nadzakucha iwe, Mudzi wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israyeli.