Isaiah 60:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe, osadutsanso mwa iwe, ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe pa mibadwo ndi mibadwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe, koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe cha anthu amibado yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa cangwiro cosatha, cokondweretsa ca mibadwo yambiri.