Isaiah 60:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golide, ndi m'malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira ntchito a chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa, ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo. Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala. Olamulira ako adzakhala a mtendere. Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m'malo mwa citsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga citsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira nchito a cilungamo.