Isaiah 60:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chiwawa sichidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako, bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako, ndidzakhala malinga ako okuteteza ndipo udzanditamanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ciwawa sicidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzacha malinga ako Cipulumutso, ndi zipata zako Matamando.