Isaiah 60:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ako onse adzayenda m'njira zoyenera, ndipo dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya. Anthuwo ndidaŵaika ndine, ndidaŵalenga ndine, kuti aonetse ulemerero wanga kwa onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya. Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala, ntchito ya manja anga, kuti aonetse ulemerero wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala colowa cao ku nthawi zonse, nthambi yooka Ine, nchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.