Isaiah 60:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko, ndipo kafuko kakang'onong'ono kadzasanduka mtundu wamphamvu. Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika. Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wamng'ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m'nthawi yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko, kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu. Ine ndine Yehova, nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wamng'ono adzasanduka cikwi, ndi wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ici m'nthawi yace.