Isaiah 60:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yang'ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali. Ana ako aakazi adzatengedwa m'manja ngati ana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzachokera kutali, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika. Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe; ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tukula maso ako uunguze-unguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzacokera kutari, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.