Isaiah 60:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing'onozing'ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gulu la ngamira lidzakukuta, ngamira zazing'ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndi lubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako, ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai. Ndipo onse a ku Seba adzabwera atanyamula golide ndi lubani uku akutamanda Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing'ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzacokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.