Isaiah 60:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ziŵeto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwanu, nkhosa zamphongo za ku Nabayoti zidzakuthandizani pamene mudzazisoŵa. Zidzaperekedwadi pa guwa ngati nsembe. Choncho Ine Chauta ndidzapatsa Nyumba yanga ulemerero waukulu kupambana kale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu, nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani; zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe, ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.