Isaiah 60:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezo ndi zombo zochokera ku maiko akutali, za ku Tarisisi zili patsogolo. Zikudzatula ana anu amene atenga siliva ndi golide, kuti alemekeze dzina la Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, chifukwa Iyeyo adakupatsani ulemerero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako amuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali; patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi, zikubweretsa ana ako ochokera kutali, pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo, kudzalemekeza Yehova Mulungu wako, Woyerayo wa Israeli, pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisi kutenga ana ako amuna kutari, golidi wao ndi siliva wao pamodzi nao, cifukwa ca dzina la Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli, popeza Iye wakukometsa iwe.