Isaiah 61:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwakutsegulidwa kwa m'ndende;