Isaiah 61:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova; moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso, ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo. Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake, ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandibveka ine ndi zobvala za cipulumutso, nandipfunda copfunda ca cilungamo, monga mkwati abvala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.