Isaiah 61:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe nthaka imameretsa mbewu ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala, momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando pamaso pa mitundu yonse ya anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zace, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa cilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.