Isaiah 61:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa cobvala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, cobvala ca matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya cilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.